PHUNZIRO 16
Kulankhula Molimbikitsa
Yobu 16:5
MFUNDO YAIKULU: M’malo mongotchula mavuto okhaokha, muzifotokoza njira yothetsera mavutowo komanso mfundo zimene zingalimbikitse anthu.
MMENE MUNGACHITIRE:
Muziona kuti anthu amene mukulankhula nawo ali ndi mtima wabwino. Muziona kuti Akhristu anzanu amafuna kusangalatsa Yehova. Ngakhale pamene mukufuna kuwapatsa malangizo, muziyamba ndi kuwayamikira kuchokera pansi pa mtima.
Chepetsani mfundo zosalimbikitsa. Zinthu zina zosalimbikitsa mukhoza kuzitchula ngati mukufuna kutsimikizira mfundo inayake. Koma nkhani yanu yonse iyenera kukhala yolimbikitsa.
Muzigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu. Thandizani anthu kuganizira zimene Yehova wachita m’mbuyomu, zimene akuchita panopa, ndiponso zimene adzachite m’tsogolo. Thandizani anthu kukhala ndi chiyembekezo komanso kuti alimbe mtima.