NYIMBO 96
Baibulo Ndi Chuma
zosindikizidwa
1. Pali buku limene mawu ake
Amatibweretsera chimwemwe.
Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu,
Limapatsa nzeru owerenga.
Bukuli ndi Baibulo loyera.
Olilemba anauziridwa.
Ankakonda Yehova M’lungu wawo,
Mzimu wake unawathandiza.
2. Analemba zokhudza chilengedwe,
Mmene M’lungu anachilengera.
Analembanso za Paradaiso
Ndiponso za mmene anathera.
Analemba za mngelo winawake
Amene ananyoza Yehova.
Anabweretsa mavuto pa anthu
Koma Yehova adzapambana.
3. Masiku ano tikusangalala
Ufumu wa Mulungu wayamba.
Tiuze anthu uthenga wabwino
Ndi madalitso omwe abwere.
M’Baibulo muli zosangalatsa.
Chakudya chochuluka kwambiri.
Limatipatsa mtendere wambiri,
Tiyesetse kumaliwerenga.
(Onaninso 2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21.)