NYIMBO 106
Khalani Achikondi
zosindikizidwa
1. M’lungu tikupempha m’tipatse,
Makhalidwe anu onsewo.
Koma lofunika koposa
N’chikondi, mzimu ’matipatsa
Tingakhaletu ndi maluso,
Popanda chikondi n’ngachabe.
Tisonyezanedi chikondi,
M’zochita ndi muzolankhula.
2. Chikondi chimatithandiza
Kuti tikhaledi opatsa.
Sichimasunganso zifukwa,
Chimakhululukira ena.
Chikondi chimapiriranso,
Mavuto angakule bwanji.
Chikondi sichimagonjanso;
Chidzakhala mpaka muyaya.
(Onaninso Yoh. 21:17; 1 Akor. 13:13; Agal. 6:2.)