NYIMBO 107
Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu
zosindikizidwa
1. Yehova M’lungu, n’chitsanzo chabwino
Inde cha chikondi.
Zochita zake, zimatithandiza
Kuti tizimutsanzira.
Anatipatsa, Mwana wake Yesu
Kuti tikhululukidwe zolakwa.
Monga umboni wa chikondi chake
M’lungu wathu, ndiye chikondi.
2. Tikatsanzira M’lungu tisonyeza
Chikondi choona,
Abale onse, tidzawathandiza
Mosasankha aliyense.
Tikonde M’lungu komanso anzathu,
Chimenechi ndi chikondi choona.
Tizikwirira zolakwa za ena,
Tidzasonyezadi chikondi.
3. Chikondi chathu chimatithandiza
Kumagwirizana.
Atate wathu akupempha kuti:
‘Dzalaweni mgwirizano.’
Musangalale n’chikondi choona;
Mawu a M’lungu amatiyengatu.
Abale athu, amatikumbutsa,
Za chikondi cha M’lungu wathu.
(Onaninso Aroma 12:10; Aef. 4:3; 2 Pet. 1:7.)