NYIMBO 67
“Lalikira Mawu”
zosindikizidwa
1. Mulungu watilamula;
Ndipo tikufunika kumvera.
Tifotokozeretu anthu
Adziwe chiyembekezo chathu.
(KOLASI)
Lalikira
Indetu onse amve!
Lalika,
Dzikoli lisanathe.
Lalika,
Ofatsa amvetsetse.
Lalika
M’dziko lonse!
2. Mavuto adzatiyesa;
Tingapezeke tikunyozedwa.
Kulalikira kungavute,
Tidzakhulupirirabe M’lungu.
(KOLASI)
Lalikira
Indetu onse amve!
Lalika,
Dzikoli lisanathe.
Lalika,
Ofatsa amvetsetse.
Lalika
M’dziko lonse!
3. Nthawi zina tidzapeza,
Anthu ofunadi kumvetsera.
Tiwaphunzitsa ’pulumuke
Dzina la Yehova tiyeretse.
(KOLASI)
Lalikira
Indetu onse amve!
Lalika,
Dzikoli lisanathe.
Lalika,
Ofatsa amvetsetse.
Lalika
M’dziko lonse!
(Onaninso Mat. 10:7; 24:14; Mac. 10:42; 1 Pet. 3:15.)