NYIMBO 131
“Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
zosindikizidwa
1. Mulungu ndi anthu,
Amva malonjezo.
Chingwe cholimba bwino,
Chamangidwa lero.
(KOLASI 1)
Mwamuna walonjeza
Kukonda mkaziyu.
“Chomwe M’lungu wamanga,
Musalekanitse.”
2. Onse afufuza
M’Mawu a Mulungu,
Kuti akwaniritse,
Zomwe alonjeza.
(KOLASI 2)
Mkaziyu walonjeza
Kukonda mwamuna.
“Chomwe M’lungu wamanga,
Musalekanitse.”
(Onaninso Gen. 2:24; Mlal. 4:12; Aef. 5:22-33.)