NYIMBO 114
“Khalani Oleza Mtima”
zosindikizidwa
1. Mbuye wathu Yehova,
Dzina lake ndi loyera.
Amafunitsitsatu
Kuliyeretsa dzinali.
Mumibadwo yambiri,
Iye ndi wopirira;
Amalezanso mtima,
Ndipo sakutopa.
Cholinga chake n’choti
Anthu adzapulumuke.
Adzapitirizabe
Kukhala woleza mtima.
2. Tikamaleza mtima
Tidzamvera M’lungu wathu.
Khalidweli n’labwino,
Timatha kupewa mkwiyo.
Timaona zabwino
Mwa ena nthawi zonse.
Limatithandizanso
Pa mavuto onse.
Makhalidwe enanso
Omwe n’zipatso zamzimu,
Adzatithandizadi
Kutsanzira M’lungu wathu.
(Onaninso Eks. 34:14; Yes. 40:28; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Tim. 2:4.)