NYIMBO 28
Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova
zosindikizidwa
1. Ndani angakhale
bwenzi lanu M’lungu?
Ndani mungam’khulupirire,
Angakhale mnzanu?
Ndi onse amene,
Amakukondani,
Amakukhulupirirani,
Okonda cho’nadi.
2. Ndani angakhale
bwenzi lanu M’lungu?
Ndani angafike kumpando
wanu wachifumu?
Ndi onse amene,
Amakumverani,
Olemekeza dzina lanu
Okulambirani.
3. Timakuuzani,
Zamumtima mwathu,
Ndipo timamva
Kuti tili pafupidi nanu.
Tifuna kukhala.
Mabwenzi a inu.
Palibiretu bwenzi,
Lomwe lingakuposeni.
(Onaninso Sal. 139:1; 1 Pet. 5:6, 7.)