NYIMBO 94
Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake
zosindikizidwa
1. Yehova Atate, tikuthokoza
Chifukwa Mawu anu mwatipatsa.
Munawauziradi;
Anatimasula.
Kuwala kwake kwatipatsa nzeru.
2. Mawu anu ndi amphamvu kwambiri.
Maganizo n’zolinga ’lekanitsa.
Ndiponso malamulo,
Anu n’ngolungama.
Mfundo zanu zimatitsogolera.
3. Mawu anu M’lungu, amatikhudza.
Aneneri anu anali anthu,
Chonde tithandizeni
Tikhulupirire.
Mwatipatsa Mawu, tathokoza Ya.
(Onaninso Sal. 19:9; 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)