NYIMBO 17
“Ndikufuna”
zosindikizidwa
1. Khristu anasonyezatu,
Chikondi, kukoma mtima.
Pobwera padziko,
n’kutithandiza
M’mawu komanso zochita;
Ankakonda ovutika
Anachiritsa odwala.
Ndi kukwaniritsa ntchito yake
Ananena: “Ndikufuna.”
2. Tifuna kumutsanzira
M’zonse zomwe timachita.
Timasonyezatu
kukoma mtima,
Pophunzitsa ’nthu kumvera.
Anzathu akavutika;
Tiwasonyeze chikondi.
Choncho amasiye akapempha.
Tidzanena: “Ndikufuna.”
(Onaninso Yoh. 18:37; Aef. 3:19; Afil. 2:7.)