NYIMBO 24
Bwerani Kuphiri la Yehova
zosindikizidwa
1. Phiri la Yehova,
Tangoliyang’anani.
Latalika kuposa
Ena onse lero.
Anthu akubwera,
Kuchokera kutali,
Akuitanizana,
‘Bwerani kwa M’lungu.’
Tsopano wamng’ono
Wakhala mtundu waukulu,
Tikuona kuti,
Tikudalitsidwa ndi M’lungu.
Ambiri tsopano
Akuvomerezadi.
Ulamuliro wake
Mokhulupirika.
2. Yesu walamula
Kuti tipite ndithu.
Tikalalikire
Uthenga wa Ufumu.
Khristu wayambano
Ulamuliro wake.
Iye akuti tikhale
Kumbali yake.
Ndi zosangalatsa,
Kuona khamu lalikulu.
Likukulirabe,
Ndipo tonse tikuthandiza.
Tonse tifuule,
Tiitanetu anthu,
‘Bwerani kuphiri
la Yehova Mulungu.’
(Onaninso Sal. 43:3; 99:9; Yes. 60:22; Mac. 16:5.)