HAGAI ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Anadzudzula anthu chifukwa chosamanganso kachisi (1-11) ‘Kodi ino ndi nthawi yoti inu muzikhala mʼnyumba zokongoletsedwa ndi matabwa?’ (4) “Ganizirani mofatsa zimene mukuchita” (5) Kudzala zambiri nʼkukolola zochepa (6) Anthu anamvera mawu a Yehova (12-15) 2 Kachisi wachiwiri adzadzaza ndi ulemerero (1-9) Kugwedeza mitundu yonse ya anthu (7) Zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu ya anthu zidzabwera (7) Madalitso obwera chifukwa chomanganso kachisi (10-19) Chopatulika sichingachititse kuti chodetsedwa chikhale chopatulika (10-14) Uthenga wopita kwa Zerubabele (20-23) “Ndidzachititsa kuti ukhale ngati mphete yodindira” (23)