Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lff 71
  • Kodi Ndakonzeka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndakonzeka?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Kodi Ndakonzeka Kulalikira Limodzi Ndi Mpingo?
  • Kodi Ndakonzeka Kubatizidwa?
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff 71

Kodi Ndakonzeka?

zosindikizidwa

Kodi Ndakonzeka Kulalikira Limodzi Ndi Mpingo?

Mukhoza kukhala wofalitsa wosabatizidwa ngati . . .

  • Nthawi zonse mumawerenga Baibulo, mumapemphera komanso mumachita nawo misonkhano yampingo.

  • Mumakonda ndi kukhulupirira zomwe mukuphunzira ndipo mukufuna kuyamba kuuzako anthu ena.

  • Mumakonda Yehova komanso mumacheza ndi anthu omwe amamukonda.

  • Munafufutitsa dzina lanu ndiponso kusiyiratu kuchita zinthu zokhudza ndale komanso chipembedzo chonyenga.

  • Mumatsatira mfundo za Yehova pa moyo wanu ndiponso mukufuna kukhala wa Mboni za Yehova.

Wophunzira Baibulo ali ndi mphunzitsi wake ndipo akulalikira mayi wina yemwe amupeza panyumba pake.

Ngati mukuona kuti mwakonzeka kuyamba kulalikira limodzi ndi mpingo, amene amakuphunzitsani Baibulo angakonze zoti mukumane ndi akulu n’cholinga choti akuuzeni zoyenera kuchita.

Kodi Ndakonzeka Kubatizidwa?

Mukhoza kubatizidwa ngati . . .

  • Ndinu wofalitsa wosabatizidwa.

  • Mumayesetsa kulalikira nthawi zonse.

  • Mumamvera komanso kutsatira malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mateyu 24:45-47.

  • Munadzipereka kwa Yehova m’pemphero ndipo mukufuna kumutumikira mpaka kalekale.

Wophunzira Baibulo akubatizidwa pamsonkhano wa Mboni za Yehova.

Ngati mukuona kuti mwakonzeka kubatizidwa, amene amakuphunzitsani Baibulo angakonze zoti mukumane ndi akulu n’cholinga choti akuuzeni zoyenera kuchita.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani