LAYIBULARE YA PA INTANETI
Watchtower
LAYIBULARE YA PA INTANETI
Chitonga (Malawi)
  • BAYIBOLU
  • MABUKU
  • MAUNGANU
  • mwbr24 March pp. 1-12
  • Malifalensi nga “Nkhani za Unganu wa Umoyu Widu Ndipuso Uteŵeti”

Vidiyo yo mwasankha palivi.

Pepani, vidiyo iyi yikana kujula.

  • Malifalensi nga “Nkhani za Unganu wa Umoyu Widu Ndipuso Uteŵeti”
  • Malifalensi nga Nkhani za Unganu wa Umoyu Widu Wachikhristu Ndipuso Uteŵeti—2024
  • Mitu yimanayimana
  • MARCH 4-10
  • MARCH 11-17
  • MARCH 18-24
  • MARCH 25-31
  • APRIL 1-7
  • APRIL 8-14
  • APRIL 15-21
  • APRIL 22-28
  • APRIL 29–MAY 5
Malifalensi nga Nkhani za Unganu wa Umoyu Widu Wachikhristu Ndipuso Uteŵeti—2024
mwbr24 March pp. 1-12

Malifalensi nga Nkhani za Unganu wa Umoyu Widu Ndipuso Uteŵeti

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

MARCH 4-10

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 16-17

“Yehova, Chisimi Changu cha Vinthu Vamampha”

w18.12 26 ¶11

Achinyamata, Mungakondwa ndi Umoyu

MUSANIYENGI ANYINU AMAMPHA

11 Ŵerengani Sumu 16:3. Davidi waziŵanga vo vingatiwovya kusaniya anyidu amampha. Iyu ‘wakondwanga ukongwa’ kucheza ndi ŵanthu wo ayanjanga Yehova. Davidi wangukamba kuti anyaki wo wachezanga nawu ŵenga “atuŵa” chifukwa ayesesanga kuja ndi mijalidu yamampha. Munthu munyaki so yo wakulembaku buku la Sumu wanguti: “Nde mubwezi wa ŵanthu wo atikuwopani ndi wo asunga marangu nginu.” (Sumu 119:63) Nge mo tinguwone mu nkhani ya sabata yamala, namwi mungasaniya anyinu amampha pa gulu la ŵanthu wo atopa Yehova ndi kumuvwiya. Mungakorana ubwezi ndi anamana anyinu kweniso ndi arara.

w14-CN 2/15 29 ¶4

“Tiziona Ubwino wa Yehova”

“Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso chikho changa. Inu mukundisungira bwino kwambiri cholowa changa. Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.” (Sal. 16:5, 6) Davide ankayamikira kwambiri “gawo” lake, kapena kuti mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso womutumikira. Mofanana ndi Davide, ife timakumana ndi mavuto ambiri koma tadalitsidwanso m’njira zambiri. Choncho tiyeni tipitirize kusangalala potumikira Mulungu woona komanso ‘kuyang’ana moyamikira’ kachisi wauzimu wa Yehova.

w08-CN 2/15 3 ¶2-3

Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse

2 Tonsefe timaphunzira zambiri pankhani za anthu odziwika bwino a m’Baibulo monga Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Davide, Estere, mtumwi Paulo ndi ena. Komanso tingapindule ndi nkhani za anthu omwe si odziwika kwambiri. Kusinkhasinkha nkhani za m’Babulo kungatithandize kuchita zimene wamasalmo anachita. Iye anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse: Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Sal. 16:8) Kodi mawuwa akutanthauza chiyani?

3 Kale msilikali anali kugwirira lupanga kudzanja lake lamanja. Chifukwa cha zimenezi, mbali ya kumanjayo inali yosatetezeka ndi chishango chomwe anali kunyamula ku dzanja lamanzere. Komabe, iye anali kukhala wotetezeka ngati msilikali mnzake akumenya nkhondo ataima chapafupi kudzanja lake lamanja. Ifenso tikamakumbukira Yehova ndi kuchita chifuniro chake nthawi zonse, adzatiteteza. Choncho tiyeni tione mmene nkhani za m’Baibulo zingalimbitsire chikhulupiriro chathu kuti ‘tiike Yehova patsogolo pathu nthawi zonse.’

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

it-2 714

Mboni ya Jisu

Mazu nga Chiheberi ngakuti ʼi·shohnʹ (Dt 32:10; Nth 7:2), asani ngagwiriskikiya ntchitu limoza ndi mazu ngakuti ʽaʹyin (jisu) ngang’anamuwa “kamwana kanthulumi kajisu.” Mwakuyanana ŵaka, mazu ngakuti bath (mwana munthukazi) ngo nge pa Chitenje 2:18 akungagwiriskiya ntchitu pakukamba za “mwana munthukazi wa jisu,” mazu ngosi ngenanga ngakamba za mboni ya jisu. Mazu yanga (ʼi·shohnʹ bath-ʽaʹyin) ngakonkhoskeka umampha pa Salimo 17:8, kung’anamuwa, “mwana munthulumi, mwana munthukazi wa jisu” (“mboni ya jisu,” NW). Viwoneka kuti akambanga venivi chifukwa cha kachithuzi ko kawoneka mu jisu la munthu asani walelesa munyaki.

Jisu liswera cha kuziŵa asani mmasu mwasere kanthu chinanga lingaŵa sisi pamwenga kachiswaswa. Chigaŵa cha jisu cho chibenekere mboni ya jisu chikhumbika kuchivikiliya kweniso kuchiphwere chifukwa asani chigaŵa chenichi chanangika pamwenga kukoleka ndi matenda, munthu wangasuzgika kuwona pamwenga wangaleke limu kuwona. Bayibolu ligwiriskiya ntchitu mazu ngakuti “mboni ya mujisu laku” pakukamba va chinthu cho chikhumbika kuchivikiliya ukongwa. Ndimu so tikhumbika kuchitiya ndi marangu ngaku Chiuta. (Nth 7:2) Pankhani ya mo Chiuta waphweriyanga Ayisirayeli nge da, lemba la Dotoronome 32:10 likamba kuti Iyu waphweriyanga mtundu uwu “nge mboni ya jisu laki.” Davidi wangupemphera kwaku Chiuta kuti wamuvikiliyi kweniso wamuphwere “nge mboni ya jisu.” (Sl 17:8) Iyu wakhumbanga kuti Yehova wamuwovyi mwaliŵi asani arwani ŵaki amuyukiya. (Yeruzgiyani ndi Zek 2:8; po mazu nga Chiheberi ngakuti ba·vathʹ ʽaʹyin, “mboni ya jisu,”ngakugwiriskikiya ntchitu.)

MARCH 11-17

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | SALIMO 18

“Yehova . . . Ndiyu Watinditaska”

w09-CN 5/1 14 ¶4-5

Kodi Mafanizo a M’Baibulo Mumawamvetsa Bwino?

Baibulo limayerekezeranso Yehova ndi zinthu zina zopanda moyo. Mwachitsanzo, limati iye ndi “Thanthwe la Isiraeli,” “thanthwe,” ndiponso “linga.” (2 Samueli 23:3; Salmo 18:2; Deuteronomo 32:4) Kodi zinthu zimenezi zikufanana bwanji ndi Yehova? Monga mmene thanthwe lilili lolimba ndiponso losasunthika, Yehova Mulungu ndiye chitetezo chathu cholimba ndiponso chosasunthika.

5 M’buku la Masalmo muli mafanizo ambiri amene amalongosola makhalidwe osiyanasiyana a Yehova. Mwachitsanzo, Salmo 84:11 limanena kuti Yehova ali ngati “dzuwa ndi chikopa,” chifukwa chakuti iye amatipatsa kuunika, moyo, mphamvu ndiponso amatiteteza. Komanso, Salmo 121:5 limati “Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.” Anthu amene amam’tumikira, Yehova amawateteza ku mavuto otentha kwambiri ngati dzuwa, mofanana ndi mmene mthunzi umatetezera munthu kuti asapse ndi dzuwa. Amachita zimenezi powaphimba ndi mthunzi wa “dzanja” lake kapena wa “mapiko” ake.—Yesaya 51:16; Salmo 17:8; 36:7.

it-2 1161 ¶7

Mazu

Chiuta watuvwa mazu nga ateŵeti ŵaki. Ŵanthu wosi wo ateŵete Chiuta mu mzimu ndi mu uneneska asimikiza kuti Chiuta watiŵavwa asani atimupempha muchineneru chechosi cho angalongoro. Kusazgiyapu po, chinanga munthu wangapemphera chamumtima, Chiuta yo waziŵa mitima ya ŵanthu ‘watuvwa’ pamwenga wavwisiya mwakuphwere asani atimupempha. (Sl 66:19; 86:6; 116:1; 1Sa 1:13; Neh 2:4) Ŵanthu wo asuzgika asani apemphera, Chiuta wavwisiya kuti waŵawovyi. Iyu watuvwa so mazu nga ŵanthu akususka kweniso wo akhumba kuchitiya ateŵeti ŵaki vinthu viheni.—Ge 21:17; Sl 55:18, 19; 69:33; 94:9-11; Yer 23:25.

w22.04 3 ¶1

Kumbi Mungasaniya Wuli Chimangu Kweniso Likondwa Asani Mufipa Mtima?

2. Muŵanaŵaniyengi mo Yehova wangukuwovyiyanipu kuvuli. Asani mukumbuka vo vingukuchitikiyanipu kuvuli, kumbi mungaŵanaŵaniya masuzgu ngo mungufiska kukunthiyapu chifukwa chakuti Yehova ndiyu wangukuwovyani? Asani tiŵanaŵaniya mo Yehova watiwovyiyapu, kweniso mo wanguwovye ateŵeti ŵaki a mu nyengu yakali, tingaja ndi chimangu chikulu kweniso tingamuthemba ukongwa Yehova. (Salimo 18:17-19) Mura munyaki zina laki Joshua wanguti: “Nde ndi mundandanda wa mapempheru nganandi ngo Yehova wangundimuka. Venivi vandiwovya kuti ndikumbukengi nyengu zo ndingupempha Yehova vinthu chayivu ndipu wangundipaska vo ndakhumbanga.” Kukamba uneneska, asani tiŵanaŵaniya vo Yehova watichitiyapu, tisaniya nthazi zo zitovya kuti tilutirizgi kukunthiyapu asani tifipa mtima.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

it-1 432 ¶2

Akerubi

Akerubi ŵenaŵa ŵenga vikozgu vo ŵanthu akali asopanga cha nge mo ŵanthu anyaki akambiya. Mwakuyanana ndi ukaboni unyaki, akerubi ŵenaŵa awonekanga nge ŵanthu kweni (Bayibolu likambapu chechosi cha pankhani iyi). Akerubi ŵenaŵa anguŵajoba mwalusu ukongwa ndipu amiyanga angelu aunkhankhu kweniso anguŵapanga “mwakulondo pulanu” yo Yehova wangupaska Mozesi. (Ek 25:9) Wakutumika Paulo wanguŵakonkhoska kuti “akerubi aunkhankhu wo abenekeriyanga chibenekeleru chakupepesiyapu maubudi.” (Ah 9:5) Akerubi ŵenaŵa amiyanga kuŵapu kwaku Yehova. Ndipu iyu wangukamba kuti: “Ndazamuwoneke kwaku yiwi kweniko, ndipu ndazamulongoro nawi kutuliya pachanya pa chibenekeleru, ndipu kutuliya pakati pa akerubi ŵaŵi wo ŵe pabokosi la Ukaboni.” (Ek 25:22; Nu 7:89) Mwaviyo, Yehova wakambika kuti “waja pampandu waufumu pachanya pa akerubi.” (1Sa 4:4; 2Sa 6:2; 2Mf 19:15; 1Mb 13:6; Sl 80:1; 99:1; Yes 37:16) Mwakuyeruzgiya, akerubi ateŵetiyanga nge “chikozgu cha galeta” laku Yehova lo wakwerapu (1Mb 28:18), ndipu mapapa nga akerubi ngawovyanga pakuvikiliya ndipuso pakwenda mwaliŵiliŵi. Mwaviyo Davidi, pakulemba mu sumu yaki yandakatulu, wangukonkhoska mo Yehova wasikiya mwaliŵiliŵi kuti watiwovyi, iyu wachita venivi ngekuti wakwera pakerubi ndipu watuza wachiphululuka chinanga “mphamapapa nga mzimu.”—2Sa 22:11; Sl 18:10.

MARCH 18-24

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 19-21

“Vakuchanya Vipharazga Unkhankhu Waku Chiuta”

w04-CN 1/1 8 ¶1-2

Anthu Onse Alengeze Ulemerero wa Yehova

DAVIDE, mwana wa Jese, anakula monga mbusa ku dera la ku Betelehemu. Ayenera kuti nthaŵi zambiri ankayang’anitsitsa kumwamba kodzaza ndi nyenyezi zambirimbiri usiku, kunja kuli zii, akuyang’anira ziweto za atate wake m’malo odyetserako nkhosa amene ankakhala kwaokha. Mosakayikira, anakumbukira zinthu zosaiŵalika zimenezi pamene, motsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, analemba ndi kuyimba mawu ochititsa chidwi a mu Salmo 19, amene amati: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Muyeso wawo wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mawu awo ku malekezero a m’dziko muli anthu.”—Salmo 19:1, 4

2 Zakumwamba zochititsa chidwi zolengedwa ndi Yehova zimalengeza ulemerero wa Yehova usana ndi usiku popanda kulankhula, popanda mawu, popanda liwu lawo kumveka. Chilengedwe sichisiya kulengeza ulemerero wa Mulungu, ndipo tikaganizira kuti umboni wopanda mawu umenewu umapita “pa dziko lonse lapansi” kuti anthu onse okhalamo awuone, zimatichititsa kuzindikira kuti ndife ochepa mphamvu kwambiri. Komabe, umboni wopanda mawu wa chilengedwe si wokwanira. Anthu okhulupirika akulimbikitsidwa kulengeza nawo umboni umenewu ndi mawu awo. Wolemba salmo wina, amene dzina lake silinatchulidwe, anauza olambira okhulupirika kuti: “M’patseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake.” (Salmo 96:7, 8) Anthu amene ali ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova amasangalala kumvera langizo limeneli. Koma kodi kupatsa Mulungu ulemerero kumatanthauza chiyani?

w04-CN 6/1 11 ¶8-10

Chilengedwe Chimalengeza Ulemerero wa Mulungu!

8 Kenako, Davide anafotokoza chinthu china chodabwitsa m’chilengedwe cha Yehova. Anati: “Iye anaika hema la dzuŵa mmenemo [m’mwamba], ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake, likondwera ngati chimphona kuthamanga m’njira. Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira kumalekezero ake: ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.”—Salmo 19:4-6.

9 Dzuŵa ndi locheperapo poyerekezera ndi nyenyezi zina. Komabe, ndi nyenyezi yaikulu, moti mapulaneti amene amazungulira dzuŵalo amaoneka aang’ono kwambiri. Buku lina limanena kuti dzuŵa ndi lolemera matani 2 biliyoni, biliyoni, biliyoni. Kulemera kumeneku kumaposeratu kutalitali kulemera kwa mapulaneti onse amene amazungulira dzuŵa kuwaphatikiza pamodzi. Mphamvu ya dzuŵa imachititsa kuti dziko lapansili lizizungulira dzuŵalo pa mtunda wa makilomita 150 miliyoni popanda kupatuka n’kupita kutali kapena kukokeka n’kuliyandikira kwambiri. Ndi mphamvu yochepa chabe ya dzuŵa imene imafika padziko lapansi koma ndi yokwanira kuti zamoyo zikhalepobe padzikoli.

10 Pofotokoza za dzuŵa pamene ananena kuti dzuŵa ndi “chimphona” chimene chimathamanga kuchokera kumalekezero ena kufika malekezero ena masana, ndipo usiku chimakagona mu “hema.” Nyenyezi yaikulu imeneyi ikamaloŵa kumadzulo, munthu akamaiona ali padziko lapansi imaoneka ngati imapita mu “hema,” ngati kuti ikukapuma. Kum’maŵa imaoneka ngati ikutumphuka, n’kuwala kwambiri “ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake.” Popeza anali mbusa, Davide ankadziŵa kuti usiku kunali kuzizira kwambiri. (Genesis 31:40) Anali kukumbukira kuti dzuŵa linkamuchititsa kumva kutenthera mofulumira komanso kutenthetsa malo amene iye anali. Mwachionekere, silinali kutopa pa “ulendo” wake wochoka kum’maŵa kufika kumadzulo koma linali ngati “chimphona,” chokonzeka kubwerezanso ulendo wake.

g95-CN 11/8 23 ¶2

Waluso wonyalanyazidwa koposa m’Nthaŵi Yathu

Kukulitsa chiyamikiro chathu kaamba ka luso m’chilengedwe kungatithandize kudziŵa Mlengi wathu, amene ntchito zake zatizinga. Nthaŵi ina Yesu anauza ophunzira ake kuyang’anitsitsa maluŵa a mthengo omera m’Galileya. “Tapenyetsani maluŵa akuthengo,” iye anatero, “makulidwe awo; sagwiritsa ntchito kapena sapota; koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa.” (Mateyu 6:28, 29) Kukongola kwa duŵa laling’ono kungatikumbutse kuti Mulungu sali wosasamala zofuna za banja la munthu.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

it-1 1073

Chiheberi, II

Muchiheberi asani alemba chiganizu, alemba munthowa yakuti chiganizu chachiŵi chileki kuyanana ndi fundu yakwamba. Mumalu mwaki, chiganizgu cho chisazgiyaku fundu yinyaki. Mwakuyeruzgiyapu pa lemba Salimo 19:7-9 pe mazu yanga:

Dangu laku Yehova ndakufikapu,

Liweziyamu nthazi.

Vikumbusu vaku Yehova vakuthembeka,

Vitimupaska zeru yo waleka kuziŵa vinandi.

Marangu ngaku Yehova ngarunji,

Ngakondwesa mtima;

Dangu laku Yehova ndakutowa,

Lingweruska masu.

Kopa Yehova nkhwakutowa,

Kuŵengepu mpaka muyaya.

Vyeruzgu vaku Yehova vauneneska;

Kweniso vaurunji.

Chiganizu chachiŵi chechosi chivwikisa umampha fundu ya muchiganizu chakwamba; mwaviyo vigaŵa vosi viŵi ivi vitovya kuti fundu yikulu yo ye pa vesi lelosi yivwiki umampha. Asani munthu waŵerenga chiganizu chachiŵi nge chakuti “liweziyamu nthazi” kweniso “vitimupaska zeru yo waleka kuziŵa vinandi,” waziŵa kuti ‘dangu ndakufikapu’ kweniso kuti “vikumbusu vaku Yehova vakuthembeka.” Mu ndakatulu nge izi, kugaŵa viyo viganizu kutovya kuti munthu wamengepu dankha pa chiganizu chakwamba wechendaŵerengi chiganizu chachiŵi. Mwaviyo asani fundu yikonkhoskeka, viganizu vosi va mundakatulu vilembeka viŵiviŵi. Ndichu chifukwa chaki ndakatulu zenizi zikambika kuti zilembeka mwapade.

MARCH 25-31

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | SALIMO 22

Bayibolu Lingukambiya Limu Vakukwaskana ndi Nyifwa Yaku Yesu

w11-CN 8/15 15 ¶16

Anapeza Mesiya

16 Mesiya adzaoneka ngati wasiyidwa ndi Mulungu. (Werengani Salimo 22:1.) Maliko ananena kuti cha m’ma 3 koloko, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “‘Eli, Eli, lama sabachthani?’ Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: ‘Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?’” (Maliko 15:34) Ponena zimenezi, sikuti Yesu anali atasiya kukhulupirira Atate wake wakumwamba. Iye anadziwa kuti Mulungu sadzamuteteza kwa adani ake pa nthawi ya imfa yake. Unali mwayi woti Yesu asonyeze kuti adzakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene akuyesedwa. Kufuula kwa Yesu kumeneku kunakwaniritsa ulosi wa pa Salimo 22:1.

w11-CN 8/15 15 ¶13

Anapeza Mesiya

13 Davide analosera kuti Mesiya adzanyozedwa. (Werengani Salimo 22:7, 8.) Yesu atapachikidwa pamtengo wozunzikirapo ananyozedwa. Mateyu analemba kuti: “Tsopano anthu odutsa anayamba kunena mawu onyoza Yesu. Anali kupukusa mitu yawo n’kumanena kuti: ‘Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!’” Nawonso ansembe aakulu, alembi komanso akulu anayamba kumuchita chipongwe ndi kunena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ameneyutu ndi Mfumu ya Isiraeli, atsiketu pamtengo wozunzikirapowo kuti ife timukhulupirire. Suja amakhulupirira Mulungu? Mulunguyo am’pulumutse tsopano ngati akumufunadi. Ndi ujatu anali kunena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’” (Mat. 27:39-43) Yesu anapirira zonsezi popanda kupsa mtima kapena kubwezera. Iye ndiye chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.

w11-CN 8/15 15 ¶14

Anapeza Mesiya

14 Adzachita maere pazovala za Mesiya. Wamasalimo analemba kuti: “Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo, ndipo akuchita maere pazovala zanga.” (Sal. 22:18) Zimenezi zinachitikadi. Baibulo limanena kuti asilikali achiroma “atam’pachika [Yesu] anagawana malaya ake akunja mwa kuchita maere.”—Mat. 27:35; werengani Yohane 19:23, 24.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

w06-CN 11/1 29 ¶7

Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika

7 Pali njira zoonekeratu zimene tingalemekezere misonkhano yathu. Njira imodzi ndiyo kuimba nawo nyimbo za Ufumu. Zambiri mwa nyimbo zimenezi zinalembedwa ngati mapemphero, choncho tiyenera kuziimba mwaulemu. Pogwira mawu Salmo 22, mtumwi Paulo analemba za Yesu kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, pakati pa mpingo ndidzakutamandani ndi nyimbo.” (Aheberi 2:12) Choncho tiziyesetsa kukhala pansi tcheyamani asanatchule nyimbo imene tiimbe kenaka n’kuimba moganizira kwambiri tanthauzo la mawu a nyimboyo. Kuimba kwathu kuzisonyeza mmene wamasalmo ankamvera, amene analemba kuti: “Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.” (Salmo 111:1) Zoonadi, kuimbira Yehova zitamando n’chifukwa chimodzi chabwino kwambiri choti tizifikira mwamsanga pa misonkhano yathu n’kukhalapo mpaka pamapeto.

w03-CN 9/1 20 ¶1

Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”

Masiku ano, monga mmene zinthu zinalili kale, anthu okhulupirira amapatsidwa mwayi woti azitha kulankhula za chikhulupiriro chawo “pakati pa msonkhano.” Aliyense ali ndi mwayi woyankha mafunso amene amafunsidwa kwa omvetsera pa misonkhano ya mpingo. Musamapeputse mphamvu ya ndemanga zimenezi. Mwachitsanzo, ndemanga zimene zimasonyeza zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto kapena tiwapeŵe zimalimbikitsa abale kuti apitirizebe kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ndemanga zofotokoza malemba a m’Baibulo amene atchulidwa koma sanawagwire mawu pandimepo, kapena zofotokoza mfundo zimene munthu wapeza atachita kafukufuku payekha, zingalimbikitse ena kukulitsa chizoloŵezi chophunzira paokha.

APRIL 1-7

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 23-25

“Yehova Ndi Mliska Wangu”

w11-CN 5/1 31 ¶3

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

Yehova amatsogolera nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimasochera. N’chimodzimodzinso anthufe, pa moyo wathu timafunika wotitsogolera. (Yeremiya 10:23) Davide anafotokoza kuti Yehova amatsogolera anthu ake “m’mabusa a msipu wambiri,” ndi “m’malo opumira a madzi ambiri.” Amawatsogoleranso “m’tinjira tachilungamo.” (Vesi 2 ndi 3) Zimene Yehova amachitazi zikufanana ndi zimene m’busa amachita posamalira nkhosa zake ndipo zikutitsimikizira kuti tiyenera kumukhulupirira. Tikamatsatira malangizo a Mulungu opezeka m’Baibulo, tingakhale ndi moyo wokhutira, wosangalala ndiponso tingakhale ndi tsogolo labwino.

w11-CN 5/1 31 ¶4

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

Yehova amateteza nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimachita mantha komanso zimasowa wozithandiza. Yehova amauza anthu ake kuti asachite mantha ngakhale ‘poyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani.’ Imeneyi ingakhale nthawi imene munthu amaona kuti ali pa mavuto adzaoneni. (Vesi 4) Pa nthawi imeneyi Yehova amaona zimene zikuchitikira atumiki ake ndipo amakhala wokonzeka kuwathandiza. Iye amapatsa atumiki ake nzeru ndi mphamvu kuti athe kupirira mayesero awo.—Afilipi 4:13; Yakobo 1:2-5.

w11-CN 5/1 31 ¶5

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

Yehova amadyetsa nkhosa zake. Nkhosa zimadalira m’busa wawo kuti azipezere chakudya. Anthufe tili ndi zosowa zauzimu zimene Mulungu yekha ndi amene angatithandize kuti tizipeze. (Mateyu 5:3) Tikuyamikira kuti Yehova ndi Wowolowa manja ndipo amapatsa atumiki ake chakudya chauzimu chambiri. (Vesi 5) Tikamawerenga zinthu monga Baibulo komanso mabuku othandiza anthu kuphunzira Baibulo, ngati Nsanja ya Olonda imene mukuwerengayi, timapeza chakudya chauzimu chimene chimatithandiza kudziwa cholinga cha moyo komanso zimene Mulungu akufuna kudzatichitira.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

w11-CN 2/15 24 ¶1-3

Muzikonda Chilungamo ndi Mtima Wanu Wonse

YEHOVA akutsogolera anthu ake “m’tinjira tachilungamo” kudzera m’Mawu ake ndiponso mwa mzimu wake woyera. (Sal. 23:3) Komabe popeza anthufe ndife opanda ungwiro, nthawi zina timachoka panjira yachilungamo. Zikatere pamafunika khama kuti tiyambirenso kuchita zinthu zabwino. Kodi chingatithandize n’chiyani? Mofanana ndi Yesu, tiyenera kukonda kuchita zinthu zolungama.—Werengani Salimo 45:7.

2 Kodi palembali “tinjira tachilungamo” n’chiyani? “Tinjira” timeneti ndi moyo umene munthu amakhala chifukwa chotsatira mfundo zolungama za Yehova. Mawu achiheberi ndiponso achigiriki amene amamasuliridwa kuti “chilungamo” amatanthauza “kuwongoka” potsatira kwambiri makhalidwe abwino. Popeza Yehova ndi “malo okhalamo chilungamo,” anthu amene amamulambira amadalira iyeyo kuti awauze njira za makhalidwe abwino zimene iwowo ayenera kutsatira.—Yer. 50:7.

3 Kuti tikondweretsedi Mulungu, tiyenera kuyesetsa ndi mtima wathu wonse kutsatira zimene iye amaona kuti ndi zolungama. (Deut. 32:4) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira zambiri za Yehova Mulungu kuchokera m’Mawu ake, Baibulo. Tikamaphunzira zambiri za Mulungu ndiponso kumuyandikira tsiku lililonse, m’pamenenso timakonda kwambiri chilungamo chake. (Yak. 4:8) Komanso tikamasankha zinthu zofunika pa moyo wathu, tiyenera kulola kuti Mawu ouziridwa a Mulungu azititsogolera.

APRIL 8-14

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 26-28

Vo Davidi Wachitanga Kuti Walutirizgi Kuja Wakugomezgeka Kwaku Yehova

w04-CN 12/1 14 ¶8-9

Yendani mu Umphumphu

8 Davide anapemphera kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” (Salmo 26:2) Impso zili m’katikati mwa thupi lathu. Impsozo, mophiphiritsira zimaimira maganizo a munthu a pansi penipeni pa mtima. Ndipo mtima wophiphiritsira umaimira m’kati mwa munthu, kapena kuti zimene zimamusonkhezera kuchita zinazake, mmene amamvera mumtima mwake, ndiponso nzeru zake. Popempha Yehova kuti amuyesere kapena kuti amuyese, Davide kwenikweni anali kupemphera kuti Yehova afufuze ndi kuyesa zoganiza zake za pansi pa mtima wake ndiponso mmene amamvera mumtima mwakemo.

9 Davide anapempha kuti impso ndi mtima wake ziyeretsedwe. Kodi Yehova amatiyeretsa motani m’kati mwathu? Davide anaimba kuti: “Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu: Usikunso impso zanga zindilangiza.” (Salmo 16:7) Kodi izi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti malangizo a Mulungu anam’fika pamtima Davide n’kukhazikika mumtimamo, ndi kukonza maganizo am’katikati mwa mtima wake. Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo ngati timasinkhasinkha ndi mtima woyamikira malangizo amene timalandira kudzera m’Mawu a Mulungu, anthu omuimira, ndiponso gulu lake, ndi kulola kuti malangizowo akhazikike mumtima mwathu. Kupemphera nthawi zonse kwa Yehova kuti atiyeretse moteremu kungatithandize kuti tiyende mu umphumphu.

w04-CN 12/1 15 ¶12-13

Yendani mu Umphumphu

12 Pofotokoza chinthu chinanso chomwe chinalimbitsa umphumphu wake, Davide anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu othyasika. Ndidana nawo msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nawo pansi ochita zoipa.” (Salmo 26:4, 5) Davide sankakhala pansi, ngakhale pang’ono chabe, ndi anthu oipa. Sankafuna kugwirizana nawo.

13 Nanga bwanji ifeyo? Kodi timakana kukhala ndi anthu achabe, kudzera m’mapulogalamu a pa TV, m’mavidiyo, m’makanema, pa Intaneti, kapena m’njira zina? Kodi timapewa anthu amene amabisa umunthu wawo? Anthu ena kusukulu kapena kuntchito kwathu anganamizire kuti ndi anzathu pamene ali ndi zolinga zachabe. Ndithudi, sitingafune kugwirizana ndi anthu amene sayenda m’choonadi cha Mulungu. Ngakhale kuti ampatuko amati ndi anthu oona mitima, nawonso angabise cholinga chawo pofuna kuti atisiyitse kutumikira Yehova. Kodi tingatani ngati mumpingo wachikristu muli ena amene ali ndi moyo wachiphamaso? Nawonso ndiye kuti amabisa umunthu wawo weniweni. Jayson, yemwe tsopano ndi mtumiki wotumikira, anali ndi anzake ngati amenewa ali wamng’ono. Pofotokoza za anthu amenewa, iye anati: “Tsiku lina mmodzi wa anzangawa anandiuza kuti: ‘Zimene timachita panopa zilibe ntchito chifukwa dziko latsopano likamadzafika, tidzakhala titafa basi. Sitidzadziwa kuti tikumanidwa chilichonse.’ Zimene ananenazi zinandigalamutsa. Ineyo sindikufuna kuti ndidzakhale nditafa dziko latsopano likamadzabwera.” Jayson anachita zanzeru posiya kugwirizana ndi anthu amenewa. Mtumwi Paulo anachenjeza motere: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Motero kupewa kugwirizana ndi anthu oipa n’kofunika kwambiri.

w04-CN 12/1 16 ¶17-18

Yendani mu Umphumphu

17 Chihema, pamodzi ndi ntchito zake za nsembe, chinali likulu lolambirirapo Yehova ku Israyeli. Pofotokoza mmene ankasangalalira ndi malo amenewo, Davide anapemphera kuti: “Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.”—Salmo 26:8.

18 Kodi timakonda kusonkhana pamalo amene timaphunzira za Yehova? Nyumba ya Ufumu iliyonse, chifukwa cha maphunziro auzimu amene amachitikirapo, imakhala likulu la kulambira koona m’dera limene muli nyumbayo. Komanso, chaka n’chaka timakhala ndi misonkhano yachigawo, yadera, ndiponso masiku a misonkhano yapadera. Pamisonkhanoyi pamafotokozedwa “mboni,” kapena kuti zikumbutso za Yehova. Tikaphunzira ‘kuzikonda kwambiri’ zikumbutsozi, timakhala ofunitsitsa kupita kumisonkhano ndi kukatchera khutu tikafika kumisonkhanoko. (Salmo 119:167) N’zotsitsimutsa kwambiri kukhala ndi okhulupirira anzathu amene amadera nkhawa za moyo wathu ndiponso amene amatithandiza kupitiriza kuyenda mu umphumphu.—Ahebri 10:24, 25.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

w06-CN 7/15 28 ¶15

Yehova Amalanditsa Wovutika

15 Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) N’zolimbikitsa kudziwa kuti chikondi cha Yehova chimaposa cha kholo lina lililonse. Ngakhale kuti kukanidwa ndiponso kuzunzidwa ndi makolo kungakhale kowawa kwambiri, sikungasinthe mmene Yehova amatisamalirira. (Aroma 8:38, 39) Kumbukirani kuti Yehova amakoka munthu yemwe wakonda. (Yohane 3:16; 6:44) Zilibe kanthu kuti anthu akhala akukuchitirani zotani, Atate wanu wakumwamba amakukondani.

APRIL 15-21

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 29-31

Chilangu Chilongo Kuti Chiuta Watitiyanja

it-1 802 ¶3

Chisku

Mazu ngakuti ‘kubisa chisku’ ngangang’anamuwa vinthu vinandi mwakukoliyana ndi mo vinthu vilili. Asani Yehova Chiuta wabisa chisku chaki vilongo kuti waleka kutiyanja pamwenga kutiwovya ndi nthazi zaki. Venivi vichitika, chifukwa cha kuleka kuvwiya kwa munthu yumoza pamwenga gulu la ŵanthu wo akwaskika nge mo venge ndi mtundu wa Ayisirayeli. (Yb 34:29; Sl 30:5-8; Yes 54:8; 59:2) Nyengu zinyaki ving’anamuwa kuti Yehova wakhumba cha kujivumbuwa mwakuchitapu kanthu mwaliŵi pamwenga kumuka po walindizga nyengu yakwenere. (Sl 13:1-3) Davidi wangupempha kuti, “Tuzganiku chisku chinu ku maubudi ngangu.” Yapa Davidi wangupempha Chiuta kuti wamugowoke pamwenga wamutuziyepu maubudi.—Sl 51:9; yeruzgiyani ndi Sl 10:11.

w07-CN 3/1 19 ¶1

Osangalala Kudikira Yehova

Njira imene chilango cha Yehova chimatipindulitsira tingaiyerekezere ndi mmene zipatso zimakhwimira. Baibulo limanena mawu otsatirawa pankhani ya kulanga kwa Mulungu: “Kwa aja amene aphunzitsidwa nako, kumabala chipatso cha mtendere, ndicho chilungamo.” (Aheberi 12:11) Zipatso zimatenga nthawi kuti zipse, motero kusintha maganizo athu kuti agwirizane ndi zimene mawu a Mulungu amatiphunzitsa, kumatenganso nthawi. Mwachitsanzo, ngati khalidwe lathu linalake losayenera litachititsa kuti titaye mwayi winawake wotumikira mumpingo, mtima wodikira Mulungu ungatithandize kuti tisafooke kwambiri n’kufika potayiratu mtima. Pamenepa, mawu ouziridwa a Davide otsatirawa angatilimbikitse: “Mkwiyo [wa Mulungu] ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.” (Salmo 30:5) Tikakhala ndi mtima wodikira ndi kutsatira malangizo a Mawu a Mulungu ndi gulu lake, nthawi yathu ya “kufuula kokondwera” idzafika.

w21.10 6 ¶18

Kumbi Kulapa Chayiku Kung’anamuwanji?

18 Kuti munthu yo wasezgeka walongo kuti walapa nadi, wakhumbika kuwungana nyengu zosi kweniso kulondo ulongozgi wo ŵara amupaska kuti wapempherengi kweniso wasambirengi Bayibolu nyengu zosi. Iyu wangakhumbika so kufwiyapu kuti wakhwechengi vinthu vo vingamuchitiska kuti wachiti so ubudi. Asani wangafwiyapu kuti wanozgi so ubwezi waki ndi Yehova, wangasimikiza kuti Yehova wamugowokiyengi nadi kweniso kuti ŵara amuweziyengi mumpingu. Pa nyengu yo ŵara afufuza kuti aziŵi asani munthu yo wanguchita ubudi walapa nadi, aziŵa kuti nkhani yeyosi yipambana ndi yinyaki. Mwaviyo, ayeruzga mwakuthaŵiriya cha kweniso mwankhaza cha.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

w06-CN 5/15 19 ¶13

Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo

31:23—Kodi munthu wodzitama amabwezeredwa motani zochuluka? Zimene akutchula pano kuti adzabwezeredwa ndi chilango. Munthu wolungama amabwezeredwa m’njira ya chilango chochokera kwa Yehova chifukwa cha zimene waphonyetsa mwangozi. Popeza munthu wodzitama sasiya kuchita zoipa, amabwezeredwa zochuluka ndi chilango chokhwima.—Miyambo 11:31; 1 Petro 4:18.

APRIL 22-28

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 32-33

Ntchifukwa Wuli Tikhumbika Kusumuwa Ubudi Ukulu?

w93-CN 3/15 9 ¶7

Chifundo cha Yehova Chimatipulumutsa Kukugwiritsidwa Mwala

7 Ngati tiri ndi liwongo la machimo aakulu a lamulo la Mulungu, tingakupeze kukhala kovuta kuulula machimo athu, ngakhale kwa Yehova. Kodi chingachitike nchiyani m’mikhalidwe yotero? Mu Salmo 32, Davide anavomereza kuti: ‘Pamene ndinakhala chete [mmalo mwakuulula] mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu [la Yehova] linandilemera ine; Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.’ (Vesi 3, 4) Kuyesa kubisa tchimo lake ndi kukanikiza chikumbumtima cha liwongo kunatopetsa Davide wochimwayo. Nkhaŵa inathetsa nyonga yake kwambiri kotero kuti anali wofanana ndi mtengo wa m’chilala wopanda madzi opatsa moyo. M’chenicheni, angakhale atakhala ndi ziyambukiro zovulaza mwa maganizo ndi mwakuthupi. Ndiiko komwe, iye anataya chisangalalo chake. Ngati aliyense wa ife agwera mumkhalidwe wofananawo, kodi tiyenera kuchitanji?

cl-CN 262 ¶8

Mulungu “Wokhululukira”

8 Davide atalapa ananena mawu aŵa: ‘Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. . . . Ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ (Salmo 32:5) Mawu akuti “munakhululukira” atembenuzidwa kuchokera ku mawu achihebri amene makamaka amatanthauza kuti “kunyamula” kapena “kutenga.” Mmene agwiritsidwira ntchito pa lembali akusonyeza kuchotsa “cholakwa, tchimo, kapena choipa.” Motero tingati Yehova ananyamula machimo a Davide n’kuwachotsa. Mosakayikira izi zinachepetsa malingaliro amene Davide anali nawo odziona kuti anali wolakwa. (Salmo 32:3) Ifenso tingakhale n’chidaliro chonse mwa Mulungu yemwe amachotsa machimo a anthu ofuna kuti awakhululukire chifukwa cha kukhulupirira kwawo nsembe ya dipo ya Yesu.—Mateyu 20:28.

w01-CN 6/1 30 ¶1

Kulapa Komwe Kumachiritsa

Davide atavomereza machimo ake sanadzione monga wopanda pake. Mawu ake m’masalmo omwe analemba onena za kuulula machimo, akusonyeza kuti anali womasuka ndi wotsimikiza kutumikira Mulungu mokhulupirika. Mwachitsanzo, taonani Salmo 32. Vesi 1 limati: “Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.” Ngakhale tchimo litakhala lalikulu bwanji, zotsatira zake zimakhala zosangalatsa ngati munthu alapa moona mtima. Njira imodzi yosonyeza kuona mtima kumeneku, ndiyo kuvomereza zomwe tachita monga anachitira Davide. (2 Samueli 12:13) Iye sanapeze zifukwa zopeputsira kuchimwa kwake kwa Yehova kapena kuyesa kuloza ena chala. Vesi 5 likuti: “Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.” Kulapa kwenikweni kumakhazikitsa mtima pansi, choncho munthu savutikanso ndi chikumbumtima chake poganiza zomwe anachita kale.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

w06-CN 5/15 20 ¶1

Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo

33:6—Kodi “mpweya” wa m’kamwa mwa Yehova n’chiyani? Mulungu amagwiritsa ntchito, kapena kuti mzimu woyera, imene anagwiritsa ntchito polenga miyamba yomwe timaonayi. (Genesis 1:1, 2) Umatchedwa mpweya wa m’kamwa mwake chifukwa chakuti, mofanana ndi kupuma mwamphamvu, mzimuwu ungathe kutumizidwa kukagwira ntchito kutali kwambiri.

APRIL 29–MAY 5

CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | MASALIMO 34-35

“Muthamikengi Yehova Nyengu Zosi”

w07-CN 3/1 22 ¶11

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

11 “Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kum’lemekeza kwake kudzakhala m’kamwa mwanga kosalekeza.” (Salmo 34:1) Popeza Davide ankakhala mothawathawa, ayenera kuti ankada nkhawa kuti azipeza bwanji zosowa za moyo wake. Koma mawu amenewa akusonyeza kuti Davide anapitirizabe kukhala ndi mtima wofuna kulemekeza Yehova, ngakhale kuti anali ndi nkhawa zimenezi. Iye alidi chitsanzo chabwino kwa ife tikamakumana ndi mavuto. Kaya tili ku sukulu, ku ntchito, tili limodzi ndi Akhristu anzathu, kapena tikulalikira, cholinga chathu chachikulu chizikhala chofuna kulemekeza Yehova. Tangoganizirani zifukwa zambirimbiri zomwe tili nazo zochitira zimenezi. Mwachitsanzo, pali zinthu zambiri zomwe tingaziphunzire ndi kusangalala nazo m’chilengedwe cha Yehova chochititsa chidwichi. Ndipo taganizirani zimene Yehova wachita pogwiritsira ntchito mbali yapadziko lapansi ya gulu lake. Yehova wagwiritsira ntchito anthu okhulupirika kuchita zinthu zazikulu, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro. Kodi ntchito za Mulungu tingaziyerekezere ndi za anthu amene dzikoli limawalambira? Kodi simukugwirizana ndi Davide, amene analemba kuti: “Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu.”—Salmo 86:8.

w07-CN 3/1 22 ¶13

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

13 “Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera.” (Salmo 34:2) Apa, Davide sanali kudzitama chifukwa cha zinthu zimene anachita bwino. Mwachitsanzo, sanadzitame chifukwa cha mmene ananamizira mfumu ya ku Gati. Anazindikira kuti Yehova anam’teteza ali ku Gati, ndi kuti anathawa chifukwa cha thandizo lake. (Miyambo 21:1) Choncho Davide sanadzitame, koma anatamanda Yehova. Zimenezi zinachititsa anthu ofatsa kuyamba kukonda Yehova. Yesu nayenso anakweza dzina la Yehova, ndipo zimenezi zinachititsanso anthu odzichepetsa ndi ophunzitsika kuyamba kukonda Yehova. Masiku ano, anthu ofatsa a m’mayiko onse akulowa mu mpingo wapadziko lonse wa Akhristu odzozedwa, womwe Yesu ndiye Mutu wake. (Akolose 1:18) Anthu ofatsawa amakhudzidwa mtima akamva dzina la Mulungu likulemekezedwa ndi atumiki ake odzichepetsa ndiponso akamvetsetsa uthenga wa m’Baibulo mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.—Yohane 6:44; Machitidwe 16:14.

w07-CN 3/1 23 ¶15

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

15 “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse.” (Salmo 34:4) Zinthu ngati zimenezi zinali zofunika kwambiri kwa Davide. Choncho anawonjezera kuti: “Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.” (Salmo 34:6) Tikakhala ndi okhulupirira anzathu, timakhala ndi mipata yambiri yofotokoza zinthu zolimbikitsa zosonyeza momwe Yehova watithandizira kupirira mavuto. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro cha okhulupirira anzathu, monga momwe zimene Davide ananena zinalimbitsira chikhulupiriro cha anthu omwe anali ku mbali yake. Anthu omwe anali ndi Davide ‘anayang’ana [Yehova] nasanguluka: ndipo pankhope pawo sipanachite manyazi.’ (Salmo 34:5) Iwo sanachite manyazi ngakhale kuti ankathawa Mfumu Sauli. Anali ndi chikhulupiriro choti Mulungu anali ndi Davide, ndipo nkhope zawo zinali zosangalala. Mofanana ndi zimenezi, anthu amene akungophunzira kumene choonadi komanso amene akhala Akhristu kwa nthawi yaitali amadalira Yehova kuti awathandize. Popeza adzionera okha Yehova akuwathandiza, nkhope zawo n’zosangalala ndipo zimasonyeza kuti ndi otsimikiza mtima kukhalabe okhulupirika.

Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu

w06-CN 5/15 20 ¶2

Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo

35:19—Kodi pempho la Davide loti asalole adani ake kum’tsinzinira likutanthauza chiyani? Kutsinzina kukanasonyeza kuti adani a Davide akusangalala chifukwa cha kuyenda bwino kwa zolinga zawo zomuchitira zoipa. Davide anapempha kuti zimenezi zisachitike.

    Mabuku nga Chitonga (1996-2025)
    Tuwanipu
    Sereni
    • Chitonga (Malawi)
    • Tumizani
    • Vo Mukhumba
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Fundu zo Mutenere Kulondo
    • Nkhani Yakusunga Chisisi
    • Kusintha Vinthu Vachisisi
    • JW.ORG
    • Sereni
    Tumizani