9 Mundipemphere kuti andigulitse phanga lake la Makipela+ limene lili m’malire a malo ake. Andigulitse pa mtengo wake wonse inu mukuona, kuti ndiikemo malemu mkazi wanga.”+
30 Ndithu mukandiike m’phanga limene lili m’munda wa Makipela, umene uli moyang’anana ndi munda wa Mamure, m’dziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Mhiti, kuti akhale ndi manda.+