Lamlungu, October 12
[Yehova] adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika komanso adzakulimbitsani.—1 Pet. 5:10.
Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza za amuna omwe anali ndi chikhulupiriro cholimba. Koma si nthawi zonse pamene iwo ankadzimva choncho. Mwachitsanzo, nthawi zina Mfumu Davide ankadziona kuti anali “wamphamvu ngati phiri,” koma nthawi zina ‘ankachita mantha.’ (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali ndi mphamvu zapadera mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, ankadziwa kuti popanda kuthandizidwa ndi Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:5, 6; 16:17) Amuna okhulupirikawa ankakhala ndi mphamvu chifukwa chakuti Yehova ndi amene ankawapatsa mphamvuzo. Mtumwi Paulo nayenso ankadziwa kuti ankafunika kupatsidwa mphamvu ndi Yehova. (2 Akor. 12:9, 10) Iye ankakumana ndi mavuto monga matenda. (Agal. 4:13, 14) Nthawi zina ankavutikanso kuchita zinthu zoyenera. (Aroma 7:18, 19) Ndipo nthawi zinanso ankada nkhawa kapena kuchita mantha. (2 Akor. 1:8, 9) Komabe, pamene Paulo ankakhala wofooka m’pamenenso ankakhala wamphamvu. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Yehova ankamupatsa mphamvu zimene ankafunikira kuti apirire mavuto ake. w23.10 12 ¶1-2
Lolemba, October 13
Yehova amaona mumtima.—1 Sam. 16:7.
Ngati ifenso nthawi zina timavutika ndi maganizo odziona ngati achabechabe, tizikumbukira kuti Yehova ndi amene anatikoka. (Yoh. 6:44) Iye amaona zabwino mwa ife zimene eni akefe sitiziona ndiponso amadziwa mtima wathu. (2 Mbiri 6:30) Choncho tisamakayikire akamatiuza kuti ndife amtengo wapatali. (1 Yoh. 3:19, 20) Tisanaphunzire choonadi, ambirife tinkachita zinthu zimene timadziimba nazo mlandu mpaka pano. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupirika amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi inuyo mumadziimbanso mlandu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti atumiki a Yehova okhulupirika ambiri akhala akudziimba mlandu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni akaganizira zomwe ankalakwitsa. (Aroma 7:24) N’zoona kuti Paulo analapa machimo ake n’kubatizidwa. Komabe iye anadzitchula kuti “ndine wamng’ono kwambiri pa atumwi onse” komanso “wochimwa kwambiri.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15. w24.03 27 ¶5-6
Lachiwiri, October 14
Iwo anasiya nyumba ya Yehova.—2 Mbiri 24:18.
Nkhani ya Mfumu Yehoasi ikutiphunzitsa kuti tizisankha anzathu omwe angatithandize kuti tizichita zabwino. Tizisankha anthu omwe amakonda Yehova komanso amafuna kumusangalatsa. Tisamangocheza ndi anthu amsinkhu wathu okha. Kumbukirani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi mnzake Yehoyada. Mukamasankha anzanu muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iwo amandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova? Kodi amandilimbikitsa kuti ndizitsatira mfundo zake? Kodi amakonda kulankhula za Yehova komanso choonadi chake chamtengo wapatali? Kodi amalemekeza mfundo za Mulungu? Kodi iwo amangondiuza zinthu kuti andisangalatse kapena amalimba mtima n’kundiuza zimene ndikulakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona anthu amene sakonda Yehova sayenera kukhala anzanu. Koma ngati muli ndi anzanu omwe amakonda Yehova, pitirizani kucheza nawo chifukwa azikuthandizani.—Miy. 13:20. w23.09 9-10 ¶6-7