Lolemba, October 13
Yehova amaona mumtima.—1 Sam. 16:7.
Ngati ifenso nthawi zina timavutika ndi maganizo odziona ngati achabechabe, tizikumbukira kuti Yehova ndi amene anatikoka. (Yoh. 6:44) Iye amaona zabwino mwa ife zimene eni akefe sitiziona ndiponso amadziwa mtima wathu. (2 Mbiri 6:30) Choncho tisamakayikire akamatiuza kuti ndife amtengo wapatali. (1 Yoh. 3:19, 20) Tisanaphunzire choonadi, ambirife tinkachita zinthu zimene timadziimba nazo mlandu mpaka pano. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupirika amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi inuyo mumadziimbanso mlandu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti atumiki a Yehova okhulupirika ambiri akhala akudziimba mlandu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni akaganizira zomwe ankalakwitsa. (Aroma 7:24) N’zoona kuti Paulo analapa machimo ake n’kubatizidwa. Komabe iye anadzitchula kuti “ndine wamng’ono kwambiri pa atumwi onse” komanso “wochimwa kwambiri.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15. w24.03 27 ¶5-6
Lachiwiri, October 14
Iwo anasiya nyumba ya Yehova.—2 Mbiri 24:18.
Nkhani ya Mfumu Yehoasi ikutiphunzitsa kuti tizisankha anzathu omwe angatithandize kuti tizichita zabwino. Tizisankha anthu omwe amakonda Yehova komanso amafuna kumusangalatsa. Tisamangocheza ndi anthu amsinkhu wathu okha. Kumbukirani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi mnzake Yehoyada. Mukamasankha anzanu muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iwo amandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova? Kodi amandilimbikitsa kuti ndizitsatira mfundo zake? Kodi amakonda kulankhula za Yehova komanso choonadi chake chamtengo wapatali? Kodi amalemekeza mfundo za Mulungu? Kodi iwo amangondiuza zinthu kuti andisangalatse kapena amalimba mtima n’kundiuza zimene ndikulakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona anthu amene sakonda Yehova sayenera kukhala anzanu. Koma ngati muli ndi anzanu omwe amakonda Yehova, pitirizani kucheza nawo chifukwa azikuthandizani.—Miy. 13:20. w23.09 9-10 ¶6-7
Lachitatu, October 15
Ine ndine Alefa ndi Omega.—Chiv. 1:8.
Mawu akuti alefa amapezeka kumayambiriro kwa afabeti ya Chigiriki ndipo mawu akuti omega amapezeka kumapeto. Pogwiritsa ntchito mawu akuti “Alefa ndi Omega,” Yehova anasonyeza kuti akayamba kuchita chinthu sasiya mpaka chitatheka. Atangolenga Adamu ndi Hava, Yehova anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi ndipo muziliyang’anira.” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyi zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Apa iye anafotokoza momveka bwino cholinga chake. Cholingacho chinali choti pakapita nthawi, ana a Adamu ndi Hava omwe akanakhala angwiro komanso omvera adzaze dzikoli n’kulikonza kukhala Paradaiso. Pa nthawi imeneyi m’pamene zikanakhala ngati wanena kuti “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi komanso zonse zimene zili mmenemo,” ananena mawu otsimikizira kuti cholinga chake chidzatheka. Yehova ankatsimikizira kuti cholinga chake chokhudza dziko komanso anthu sichidzalephereka. Cholingachi chikanakwaniritsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.—Gen. 2:1-3. w23.11 5 ¶13-14