Loweruka, October 11
Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati.—Yes. 26:20.
‘Zipinda zamkati’ zingatanthauze mipingo yathu. Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzatiteteza monga mmene analonjezera ngati tidzapitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Choncho panopa tiyenera kuyesetsa kuti kuwonjezera pa kulola kuchita zinthu ndi abale ndi alongo athu, tiziwakondanso. Zimenezi ndi zofunika kwambiri kuti tidzapulumuke. “Tsiku lalikulu la Yehova” lidzakhala loopsa kwa anthu onse. (Zef. 1:14, 15) Nawonso atumiki a Yehova adzakumana ndi mavuto. Ngati titakonzekereratu panopa tidzatha kukhala mosatekeseka komanso kuthandiza ena. Tidzatha kupirira mavuto alionse omwe tingakumane nawo. Abale ndi alongo athu akamadzavutika, tidzachita zomwe tingathe powasonyeza chifundo komanso kuwapatsa zimene akufunikira. Ndipo tidzagwirizana ndi abale ndi alongo athu omwe tinali titayamba kale kuwakonda. Kenako Yehova adzatidalitsa potipatsa moyo wosatha m’dziko limene simudzakhalanso mavuto alionse.—Yes. 65:17. w23.07 7 ¶16-17
Lamlungu, October 12
[Yehova] adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika komanso adzakulimbitsani.—1 Pet. 5:10.
Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza za amuna omwe anali ndi chikhulupiriro cholimba. Koma si nthawi zonse pamene iwo ankadzimva choncho. Mwachitsanzo, nthawi zina Mfumu Davide ankadziona kuti anali “wamphamvu ngati phiri,” koma nthawi zina ‘ankachita mantha.’ (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali ndi mphamvu zapadera mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, ankadziwa kuti popanda kuthandizidwa ndi Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:5, 6; 16:17) Amuna okhulupirikawa ankakhala ndi mphamvu chifukwa chakuti Yehova ndi amene ankawapatsa mphamvuzo. Mtumwi Paulo nayenso ankadziwa kuti ankafunika kupatsidwa mphamvu ndi Yehova. (2 Akor. 12:9, 10) Iye ankakumana ndi mavuto monga matenda. (Agal. 4:13, 14) Nthawi zina ankavutikanso kuchita zinthu zoyenera. (Aroma 7:18, 19) Ndipo nthawi zinanso ankada nkhawa kapena kuchita mantha. (2 Akor. 1:8, 9) Komabe, pamene Paulo ankakhala wofooka m’pamenenso ankakhala wamphamvu. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Yehova ankamupatsa mphamvu zimene ankafunikira kuti apirire mavuto ake. w23.10 12 ¶1-2
Lolemba, October 13
Yehova amaona mumtima.—1 Sam. 16:7.
Ngati ifenso nthawi zina timavutika ndi maganizo odziona ngati achabechabe, tizikumbukira kuti Yehova ndi amene anatikoka. (Yoh. 6:44) Iye amaona zabwino mwa ife zimene eni akefe sitiziona ndiponso amadziwa mtima wathu. (2 Mbiri 6:30) Choncho tisamakayikire akamatiuza kuti ndife amtengo wapatali. (1 Yoh. 3:19, 20) Tisanaphunzire choonadi, ambirife tinkachita zinthu zimene timadziimba nazo mlandu mpaka pano. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupirika amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi inuyo mumadziimbanso mlandu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti atumiki a Yehova okhulupirika ambiri akhala akudziimba mlandu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni akaganizira zomwe ankalakwitsa. (Aroma 7:24) N’zoona kuti Paulo analapa machimo ake n’kubatizidwa. Komabe iye anadzitchula kuti “ndine wamng’ono kwambiri pa atumwi onse” komanso “wochimwa kwambiri.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15. w24.03 27 ¶5-6