7 Iweyo ndi ana ako, muzichita utumiki wanu waunsembe mosamala pa chilichonse chokhudza guwa lansembe, ndiponso pa zonse zamkati, kuseri kwa nsalu yotchinga.+ Umenewu ndiwo utumiki wanu.+ Unsembewu ndikukupatsani monga mphatso, ndipo aliyense wosakhala Mlevi akayandikira pafupi aziphedwa.”+