18 Zitatero ndinadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova masiku 40, usana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinadye mkate kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita ndi kukhumudwitsa Yehova, mwa kuchita zinthu zoipa pamaso pake.+