10 Tinalanda mizinda yonse ya kudera lokwererapo, m’Giliyadi monse, m’Basana monse, mpaka ku Saleka+ ndi ku Edirei,+ mizinda ya m’dera la ufumu wa Ogi ku Basana.
12 Mafukowa anatenganso dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi+ mfumu ya Basana, imene inali kulamulira ku Asitaroti ndi ku Edirei.+ Mfumu Ogi anali mmodzi mwa Arefai otsala.+ Mose anagonjetsa anthu onsewa ndi kuwapitikitsa.+