36 Ndiyeno uwombe nsalu yotchinga+ khomo la chihema. Nsaluyo ikhale ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ya ulusi wofiira kwambiri, ndi ya ulusi wopota wabwino kwambiri.
37 Atatero anawomba nsalu yotchinga khomo la chihema. Nsaluyo inali ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+