24 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘M’mwezi wa 7,+ pa tsiku loyamba m’mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, tsiku loliza lipenga,+ tsiku la msonkhano wopatulika.+
9 Ndipo m’mwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo,+ muziliza lipenga la nyanga ya nkhosa lolira mokwera kwambiri.+ Muziliza lipenga la nyanga ya nkhosalo m’dziko lanu lonse pa tsiku lochita mwambo wophimba machimo.+