-
Numeri 16:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Iwo anaukira Mose. Oukirawo anali limodzi ndi amuna achiisiraeli okwanira 250. Iwowa anali atsogoleri a anthuwo, owaimira kumisonkhano, amuna otchuka.
-
-
Numeri 16:40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Eleazara anachita izi kuti timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli, kuti munthu aliyense amene si mbadwa+ ya Aroni asayandikire kwa Yehova+ kukafukiza nsembe. Anateronso kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi gulu lake+ anachita. Eleazara anachita zonse monga mmene Yehova anamuuzira kudzera kwa Mose.
-