-
Deuteronomo 14:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Uzidzadya zinthu zako pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake. Uzidzadya chakhumi cha mbewu zako,+ kumwa vinyo wako watsopano, kudya mafuta ako, ana oyamba a ng’ombe ndi a nkhosa zako.+ Uzichita zimenezi kuti uphunzire kuopa Yehova Mulungu wako nthawi zonse.+
-
-
Deuteronomo 16:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Pamenepo uzisangalala pamaso pa Yehova Mulungu wako,+ iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, Mlevi wokhala mumzinda wanu, mlendo wokhala pakati panu,+ mwana wamasiye*+ ndi mkazi wamasiye,+ amene ali pakati panu. Muzisangalala pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake.+
-