8 Mizinda imene mukawapatseyo ikachokere kwa ana a Isiraeli.+ Fuko limene likakhale ndi mizinda yambiri mukatengeko yambiri, ndipo fuko limene likakhale ndi mizinda yochepa mukatengeko yochepa.+ Fuko lililonse likapereke ina ya mizinda yake kwa Alevi malinga ndi cholowa chawo chimene akalandire.”