8 “‘Pamapeto pake, ndinakufikitsani kudziko la Aamori amene anali kukhala kutsidya lina la Yorodano. Iwo anayamba kumenyana nanu,+ koma ine ndinawapereka m’manja mwanu kuti mutenge dziko lawo kukhala lanu. Chotero ndinawafafaniza kuwachotsa pamaso panu.+