16 Adzatero chifukwa chakuti mwaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, ndiponso chifukwa chakuti mwapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira.+ Pamenepo, mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani+ ndipo mudzatha mwamsanga padziko labwino limene iye anakupatsani.”+