28 Cholowa chawo ndiponso malo awo okhala anali Beteli+ ndi midzi yake yozungulira. Kum’mawa kunali Naarani,+ kumadzulo kunali Gezeri+ ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Sekemu+ ndi midzi yake yozungulira, mpaka kukafika ku Gaza ndi midzi yake yozungulira.