-
Yoswa 8:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Aisiraeli anapitiriza kupha amuna ankhondo onse a ku Ai. Anawaphera kuchipululu kumene anthu a ku Aiwo anathamangitsirako Aisiraeli. Anawapha ndi lupanga mpaka kuwatha onse. Atatero, Aisiraeliwo anabwerera ku Ai, n’kukapha ndi lupanga ena onse otsala.
-