16 Mafuko a Rubeni+ ndi Gadi ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi+ kukafika kuchigwa cha Arinoni, ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a ana a Amoni.+
17 Ndinawapatsa Araba, Yorodano ndi tsidya lake la kum’mawa, kuchokera ku Kinereti*+ mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere+ imene ili m’munsi mwa Pisiga,+ kotulukira dzuwa.