12 Amunawa ananyamuka pa ulendo wawo ndipo anayenda mpaka kukafika pafupi ndi Kiriyati-yearimu+ ku Yuda, n’kumanga msasa pamenepo. N’chifukwa chake malowo amatchedwa dzina lakuti Mahane-dani+ kufikira lero. Malo amenewa ali kumadzulo kwa Kiriyati-yearimu.