4 Koma Mika anabweza ndalamazo kwa mayi ake, ndipo mayi akewo anatenga ndalama zasiliva zokwana 200 n’kuzipereka kwa wosula siliva.+ Pamenepo wosula silivayo anapanga chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Zinthu zimenezi anaziika m’nyumba ya Mika.