51 Pamenepo Davide anapitiriza kuthamanga ndipo anakaima pambali pake. Kenako anatenga lupanga la Mfilisitiyo,+ kulisolola m’chimake ndi kum’pheratu mwa kum’dula mutu.+ Afilisiti ena onse ataona kuti ngwazi yawo yamphamvu ija yafa, anayamba kuthawa.+