10 Tsopano Ezara atangomaliza kupemphera+ ndi kuvomereza machimo,+ komwe ankachita akulira ndiponso ali chogona+ patsogolo pa nyumba+ ya Mulungu woona, Aisiraeli anasonkhana kwa iye. Iwo anali mpingo waukulu kwambiri, amuna, akazi ndi ana, ndipo anali atalira kwambiri.