18 Pambuyo pake, anthu onse a m’dzikolo anapita kukachisi wa Baala n’kukagwetsa maguwa ake ansembe.+ Mafano ake anawaphwanyaphwanya,+ ndipo Mateni+ wansembe wa Baala anamupha patsogolo pa maguwa ansembewo.+
Kenako wansembe Yehoyada anaika anthu kuti aziyang’anira nyumba ya Yehova.+