12 Kenako amuna ena omwe anali atsogoleri+ a ana a fuko la Efuraimu,+ anaukira asilikali amene anabwera kuchokera ku nkhondowo. Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu ndi Amasa mwana wa Hadilai.