17 Kuwonjezera apo, Mfumu Ahazi inaduladula+ malata a m’mbali+ mwa zotengera zokhala ndi mawilo,+ n’kuchotsa mabeseni+ pamwamba pa zotengerazo. Chosungiramo madzi+ inachichotsa pamwamba pa ng’ombe zamphongo zamkuwa+ n’kuchiika pansi pomanga ndi miyala.