18 Panali pasanachitikepo pasika ngati ameneyu mu Isiraeli kuyambira m’masiku a mneneri Samueli.+ Mafumu ena onse+ a Isiraeli anali asanachitepo pasika ngati amene anachita Yosiya, ansembe, Alevi, Ayuda ndi Aisiraeli onse amene analipo, ndiponso anthu okhala mu Yerusalemu.