17 Pamwambo wotsegulira nyumba ya Mulunguyo, anapereka nsembe ng’ombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200, ndi ana a nkhosa amphongo 400. Anaperekanso mbuzi zamphongo 12 za nsembe ya machimo ya ana onse a Isiraeli mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Isiraeli.+