8 Ineyo ndaika lamulo+ lokhudza zimene muyenera kuchita ndi akulu a Ayuda amenewa pa ntchito yomanganso nyumba ya Mulungu. Amuna amenewa muziwapatsa+ ndalama mosalekeza+ zochokera pa chuma cha mfumu+ zomwe anthu a kutsidya la Mtsinje amapereka pokhoma msonkho.