20 Pamene ndinali kulankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga+ ndi machimo a anthu a mtundu wanga Aisiraeli,+ ndiponso pamene ndinali kupempha pamaso pa Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima komanso kuti akomere mtima phiri loyera la Mulungu wanga,+