9 Kenako mtumiki wake Zimiri,+ mkulu woyang’anira hafu ya magaleta, anayamba kum’konzera chiwembu. Anam’konzera chiwembucho pamene Ela anali kumwa+ mowa mpaka kuledzera kunyumba+ ya Ariza ku Tiriza. Ariza anali woyang’anira banja la mfumu ku Tirizako.