12 Ndani anayezapo madzi onse a m’nyanja pachikhatho cha dzanja lake?+ Ndani anayezapo kumwamba konse ndi dzanja lake?+ Ndani anayezapo fumbi lonse la padziko lapansi ndi mbale imodzi yokha yoyezera?+ Ndani anayezapo mapiri ndi muyezo, kapena ndani anayezapo zitunda pa sikelo?