18 Ndithu musatero ayi, koma pitirizani kulandira kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+ Kwa iye kukhale ulemerero, kuyambira panopa mpaka muyaya.+
25 kwa iyeyo, Mulungu yekhayo amenenso ndi Mpulumutsi wathu+ mwa Yesu Khristu+ Ambuye wathu, kukhale ulemerero,+ ukulu, mphamvu+ ndi ulamuliro,+ kuchokera kalekale+ kufikira panopa, mpaka ku nthawi yonse yomka muyaya.+ Ame.+