3 Pamenepo Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado+ weniweni, okwera mtengo kwambiri okwana magalamu 327. Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu ndi kupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake.+ M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo.