8 Apatuka mofulumira panjira imene ndawalamula kuyendamo.+ Iwo adzipangira fano la mwana wa ng’ombe lopangidwa ndi golide wosungunula. Akuligwadira ndi kupereka nsembe kwa fanolo, ndipo akunena kuti, ‘Aisiraeli inu, uyu ndiye Mulungu wanu amene anakutsogolerani potuluka m’dziko la Iguputo.’”+