4 Makamu onse akumwamba adzawola.+ Kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu wolembapo.+ Makamu onse akumwambawo adzafota ngati mmene masamba amafotera pamtengo wa mpesa n’kuthothoka, ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.+