6 M’kalatayo analemba kuti: “Zamveka pakati pa anthu a mitundu ina ndipo Gesemu+ akunenanso zomwezo, kuti iwe ndi Ayuda mukufuna kupanduka.+ N’chifukwa chake iwe ukumanga mpandawo, ndipo malinga ndi zimene zikumvekazi, iweyo ukufuna kukhala mfumu yawo.+