6 Yehova Mulungu wanu adzachita mdulidwe wa mitima yanu+ ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.+
33 “Pangano+ limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili:+ Ndidzaika chilamulo changa mwa iwo+ ndipo ndidzachilemba mumtima mwawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,”+ watero Yehova.